Mayi Mary Laini Kaude azaka 87 ochokera m'mudzi wa Matewere mdera la mfumu yayikulu Juma m'boma la Mulanje ali mu ululu
Mayi Mary Laini Kaude azaka 87 ochokera m'mudzi wa Matewere mdera la mfumu yayikulu Juma m'boma la Mulanje ali mu ululu pomwe anthu okwiya anawamenya usiku wa lachinayi sabata ino ati powaganizira kuti akumanga mvula.
A Catherine Namanya omwe ndi mdzukulu wa mayiwa ati anthuwa analowa m'nyumba ya mayiwa kudzera pa zenera ndikuyamba kuwagenda.
Iwo ati anthu ena oyandikira atamva phokoso la anthuwa anathamangira kunyumbayo komwe anawapulumutsa ndikuwatengela ku chipatala chaching'ono cha Namphungo ndipo anawatumiza kuchipatala chachikulu cha bomali komwe anawagoneka kwa masiku awiri akulandira thandizo.
Pakadali pano m'neneri wa apolisi m'bomali Innocent Moses wati timupase nthawi asanaikepo ndemanga pa nkhaniyi.
Polakhula ndi mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa anthu achikulire m'dziko muno la MANEPO a Andrew Kavala apempha apolisi kufufuza zankhaniyi ndikuonesetsa kuti malamulo agwira ntchito kwa anthu omwe anachita zaupanduzi.
Wolemba :Grecium Gama